Covenant Protestant Reformed Church
Bookmark and Share

Mawu a Chikhulupiriro

Ndikhulupirira Mulungu Atate wa mphamvu zonse (yonse), wakulenga za kumwamba ndi za pansi.

Ndikhulupirira Yesu Khristu, Mwana wake wobadwa yekha, Ambuye wathu (Ambuyathu), amene anapatsidwa ndi (mwa) Mzimu Woyera, nabadwa ndi Mariya namwaliyo, nasautsidwa kwa Pontio Pirato, namwalira (nafa), naikidwa m’manda, natsikira kwa akufa (helo).Tsiku lachitatu anaukanso kwa akufa, nakwera Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu Atate wa mphamvu zonse (yonse), kuchokera (kudzera) komweko adzadza kudzaweruza anthu amoyo ndi akufa.

Ndikhulupirira Mzimu Woyera. Ndikhulupirira Mpingo wopatulika wa Khristu (wa Mulungu woyera) wa kwa anthu onse, chiyanjano cha oyera mtima, kukhululukidwa kwa machimo, kuukanso kwa thupi, ndi moyo wosatha.

Copyright © 2002 - Reproduced by permission of Dr. Steven Paas